Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 32:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo kudamchera iye pamene anaoloka pa Penuwele, ndipo iye anatsimphina ndi ntchafu yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo kudamchera iye pamene anaoloka pa Penuwele, ndipo iye anatsimphina ndi ntchafu yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Dzuŵa lidamtulukira Yakobe pamene ankachoka ku Penuwele, ndipo ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyung'unyu ija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Dzuwa linamutulukira Yakobo pamene amachoka pa Penueli. Tsono ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyungʼunyu yake ija.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 32:31
19 Mawu Ofanana  

Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pake pa Iye amene wakundiona ine?


Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mzinda.


Ndipo dzuwa lidakwera padziko pamene Loti anafika ku Zowari.


Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetse, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.


Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako.


Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele.


Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.


Ndafikana potsimphina, ndipo chisoni changa chili pamaso panga chikhalire.


ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee.


Koma sanatulutse dzanja lake pa akulu a ena a Israele; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.


Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.


Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.


ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wake, ndi ukulu wake, ndipo tidamva liu lake ali pakati pa moto; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.


Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo?


Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! Popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa.


Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa