nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;
Eksodo 23:24 - Buku Lopatulika Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musagwadire milungu yawo kapena kuyipembedza. Ndipo musatsatire zinthu zomwe amachita. Koma inu mukawononge milungu yawo ndi kuphwasula malo amene amapembedzerapo. |
nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;
nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.
Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.
Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa cha Baala adachipanga atate wake.
Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yake, naigwadira, naifukizira.
Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawachotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israele.
Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israele.
Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.
Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.
Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa Ine; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.
Ndipo anatenga mwanawang'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele.
Koma sunayende m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.
Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.
Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.
Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.
mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;
nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m'malomo.
Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.