Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 26:1 - Buku Lopatulika

1 Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Musadzipangire mafano ndipo musaimike zithunzi zosema kapena miyala yachipembedzo. Musaimiritse miyala yosema mwachithunzi m'dziko mwanu kuti muziipembedza. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 26:1
30 Mawu Ofanana  

Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira;


Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.


nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.


Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema.


Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide.


Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.


Usadzipangire milungu yoyenga.


Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;


Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Pakuti ana a Israele ndi atumiki anga; iwo ndiwo atumiki anga amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lake la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera nao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.


mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;


Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.


Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.


Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake aamuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa