Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:2 - Buku Lopatulika

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa cha Baala adachipanga atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa cha Baala adachipanga atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Yoramu ankachimwira Chauta, koma kuipa kwake sikudafanefane ndi kwa bambo wake ndi kwa mai wake Yezebele. Yoramuyo adagumula fano la Baala limene bambo wake adaamanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova koma sizinafanane ndi zimene anachita abambo ndi amayi ake. Iye anachotsa fano la mwala la Baala limene abambo ake anapanga.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:2
14 Mawu Ofanana  

chifukwa cha machimo ake anachimwawo, pakuchita choipa pamaso pa Yehova; popeza anayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi m'tchimo lake anachimwa nalolo, nachimwitsa nalo Aisraele.


Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.


Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.


Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikira Baala pang'ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo amachitira Manase atate wake.


Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anati, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mai wako Yezebele?


Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.


Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.


Chifukwa ninji tsono simunamvere mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa