Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele m'Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chaka cha 18 cha ufumu wa Yehosafati m'dziko la Yuda, Yoramu mwana wa Ahabu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka khumi ndi ziŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yoramu mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda ndipo analamulira zaka khumi ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:1
5 Mawu Ofanana  

Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.


Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.


Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.


Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, kukayambana nkhondo ndi Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa