Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:3 - Buku Lopatulika

3 Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Komabe adaumirira kuchita zoipa zomwe ankachita Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adaachimwitsa nazo Aisraele, osafuna konse kuzileka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Komabe anawumirira kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo sanafune kuwaleka.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:3
20 Mawu Ofanana  

Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere panjira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje.


Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele.


koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;


Nachita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wake, ndi m'tchimo lomwelo iye akachimwitsa nalo Aisraele.


Ndipo anachimwa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi m'tchimo lake iye anachimwitsa nalo Israele.


Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke.


Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; ndipo chifanizocho chinatsalanso mu Samariya.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Pakuti anang'amba Israele, kumchotsa kunyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati; Yerobowamu naingitsa Israele asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukulu.


Nayenda ana a Israele m'zolakwa zonse za Yerobowamu, zimene anazichita osazileka;


mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.


Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.


Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa