Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:8 - Buku Lopatulika

8 nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 ndipo ankayenda motsata miyambo ya anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pamene ankafika Aisraele. Ankatsatanso miyambo yachilendo imene mafumu ena a Aisraele anali ataiyambitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 ndiponso ankatsatira miyambo ya anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika mʼdzikomo pamodzinso ndi miyambo yonse imene mafumu a Israeli anayambitsa.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:8
19 Mawu Ofanana  

Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.


Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele.


Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse.


popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.


Yudanso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israele amene adawaika.


Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba.


Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.


koma anasokonekerana nao amitundu, naphunzira ntchito zao:


Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.


Atero Yehova, Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo.


Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.


Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.


Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.


Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa