Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 18:3 - Buku Lopatulika

3 Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Musamachita zimene amachita anthu a ku Ejipito kumene munkakhala kuja, ndiponso musadzachite zimene amachita anthu a ku Kanani kumene ndikukufikitsaniko. Musatsate miyambo yao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 18:3
15 Mawu Ofanana  

nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.


koma anasokonekerana nao amitundu, naphunzira ntchito zao:


Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.


Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye mu unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao.


Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao.


Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.


Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.


ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala, siliva ndi golide, zokhala pakati pao;


Musamanena mumtima mwanu, atawapirikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Chifukwa cha chilungamo changa Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa