Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 18:4 - Buku Lopatulika

4 Muzichita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Muzichita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Muzichita zimene ndikukulamulani, ndi kutsata malamulo anga ndi kuŵamvera. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Inu muzimvera malamulo anga ndipo muzisamalitsa kutsatira malangizo anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 18:4
15 Mawu Ofanana  

Kuti asamalire malemba ake, nasunge malamulo ake. Aleluya.


Inu munatilamulira, tisamalire malangizo anu ndi changu.


Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita;


Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.


Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwachita.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu.


Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.


Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana.


Ndipo musamalire malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova.


Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo.


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwachita m'dziko limene muolokerako kulilandira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa