2 Mafumu 17:11 - Buku Lopatulika11 nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Ndipo anthuwo ankafukiza lubani ku akachisi onse, monga m'mene ankachitira anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraelewo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova. Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.