Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 19:12 - Buku Lopatulika

Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza chilekezero chake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Uŵalembere malire anthuwo pozungulira phirilo, ndipo uŵauze kuti, ‘Samalani, musakwere phiri kapena kukhudza tsinde lake. Wina aliyense akalikhudza, afa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu.

Onani mutuwo



Eksodo 19:12
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.


Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula.


ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye.


Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;


Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno.


Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzola malire a abale anu, ana a Esau okhala mu Seiri; ndipo adzakuopani; muchenjere ndithu;


Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.


Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,


Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapite njirayi kufikira lero.