Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 3:4 - Buku Lopatulika

4 Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapite njirayi kufikira lero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Potero mudzaidziŵa njira yoyenera kutsata, popeza kuti nkale lomwe kumeneko simudadzereko. Komatu tsono Bokosi lachipanganolo musaliyandikire. Pakati pa inu ndi Bokosilo pazikhala mtunda wosachepera kilomita imodzi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Potero mudzadziwa njira yoti mudzere, popeza simunayendepo njira ino nʼkale lomwe. Koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi bokosilo pakhale mtunda pafupifupi kilomita imodzi.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 3:4
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekere iye monga kale.


Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.


Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.


Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.


Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;


Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.


Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.


Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.


Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.


nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata.


Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa