Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 19:13 - Buku Lopatulika

13 dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m'phirimo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m'phirimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Wina aliyense asakhudze munthuyo, koma anthu amponye miyala kapena kumubaya. Chikhale choŵeta, chidzaphedwa; akhale munthu, adzaphedwanso. Mbetete ikamalira, anthu abwere ku phiri.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndi miyala kapena kumulasa ndi mivi. Palibe amene adzamukhudze. Palibe munthu amene adzaloledwa kukhala ndi moyo ngakhale nyama. Iwo adzayenera kuphedwa.’ Koma anthu adzapita ku phirilo akadzamva kulira kwa lipenga la nyanga yankhosa.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:13
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao.


Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.


Ndipo Mose anatulutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde paphiri.


Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.


Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno.


m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.


Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka;


pakuti sanakhoze kulola cholamulidwacho. Ingakhale nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala;


Nafulumira olalirawo nathamangira Gibea, nabalalika olalirawo, nakantha mzinda wonse ndi lupanga lakuthwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa