Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 12:18 - Buku Lopatulika

18 Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho;

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Inu simunafike ku phiri limene mungathe kulikhudza, loyaka moto wa mdima bii, la mphepo yamkuntho;

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:18
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Ndipo maonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati moto wonyeketsa pamwamba paphiri, pamaso pa ana a Israele.


Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.


Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!


Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:


Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri.


Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde paphiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.


(ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:


Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa