Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 19:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza chilekezero chake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Uŵalembere malire anthuwo pozungulira phirilo, ndipo uŵauze kuti, ‘Samalani, musakwere phiri kapena kukhudza tsinde lake. Wina aliyense akalikhudza, afa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:12
11 Mawu Ofanana  

Farao anati kwa Mose, “Choka pamaso panga! Uwonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga! Tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.”


ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa.


Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.”


Koma Mose yekha ayandikire Yehova, ndipo enawo asayandikire. Komanso anthu ena onse asakwere nawe ku phiri kuno.”


Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa mukadzatero iwo adzakhala ngati msampha pakati panu.


Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.”


Apatse anthu malamulo awa: ‘Muli pafupi kudutsa mʼchigawo cha abale anu adzukulu a Esau okhala ku Seiri. Iwowa adzachita nanu mantha koma musamale kwambiri.


Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo.


Inu simunafike ku phiri limene mungathe kulikhudza, loyaka moto wa mdima bii, la mphepo yamkuntho;


Potero mudzadziwa njira yoti mudzere, popeza simunayendepo njira ino nʼkale lomwe. Koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi bokosilo pakhale mtunda pafupifupi kilomita imodzi.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa