Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.
Eksodo 15:22 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose adatsogolera Aisraele ku Nyanja Yofiira kuja nakaloŵa m'chipululu cha Suri. Adayenda m'menemo masiku atatu, osapeza madzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi. |
Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.
Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.
Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.
Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga mu Mara.
Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito.
Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.