Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 25:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Zidzukulu za Ismaeleyo zinkakhala m'dziko la pakati pa Havila ndi Suri, kuvuma kwa Ejipito, pa njira ya ku Asiriya. Zinkakhala molekana ndi zidzukulu zina za Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 25:18
17 Mawu Ofanana  

ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani.


Ndi ana aamuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani.


Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.


Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.


Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse.


Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.


Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide;


Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.


Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.


ndi Ofiri, ndi Havila, ndi Yobabu. Awa onse ndiwo ana a Yokotani.


Ansembe ao anagwa ndi lupanga; ndipo amasiye ao sanachite maliro.


Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi.


a ku Babiloni, ndi Ababiloni, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasiriya onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo.


Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa