Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.
Eksodo 14:10 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Farao atayandikira, Aisraele aja adaona Aejipito akuŵalondola, ndipo adachita mantha kwambiri, nayamba kulira mofuula kwa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Farao anayandikira. Ndipo Aisraeli ataona kuti Aigupto akuwatsatira, anachita mantha aakulu ndipo anafuwula kwa Yehova. |
Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.
Ndipo munapenya msauko wa makolo athu mu Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira,
Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.
Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba.
Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.
Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;
Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.
Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!
Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m'dziko la Ejipito, kufikira munalowa m'malo muno munapikisana ndi Yehova.
Ndipo ndinatulutsa atate anu mu Ejipito; ndipo munadza kunyanja; koma Aejipito analondola atate anu ndi magaleta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.
Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine mu Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri.
Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.