Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 81:7 - Buku Lopatulika

7 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamene munali m'mavuto mudandiitana, Ine nkukupulumutsani. Ndidakuyankhani ndili wobisika m'bingu. Ndidakuyesani ku madzi a Meriba aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani, ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu; ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 81:7
16 Mawu Ofanana  

Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.


Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.


Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m'dziko la Ejipito.


Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.


Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.


Ndipo za Levi anati, Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu, amene mudamuyesa mu Masa, amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;


Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa