Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 81:6 - Buku Lopatulika

6 Ndinamchotsera katundu paphewa pake, manja ake anamasuka ku chotengera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndinamchotsera katundu paphewa pake, manja ake anamasuka ku chotengera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Ndidakutulani katundu wa pamapeŵa panu. Manja anu ndidaŵachotsera ntchito yonyamula madengu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo; Manja awo anamasulidwa mʼdengu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 81:6
9 Mawu Ofanana  

Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala mu Netaimu, ndi mu Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m'ntchito yake.


M'mene Israele anatuluka ku Ejipito, nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo;


Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.


Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.


nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.


Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta.


Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.


Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa