Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 81:5 - Buku Lopatulika

5 Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adalipereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene zinkatuluka m'dziko la Ejipito. Ndikumva liwu limene sindidalimve ndi kale lonse, lakuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto, kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 81:5
17 Mawu Ofanana  

M'mene Israele anatuluka ku Ejipito, nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo;


Munaombola anthu anu ndi mkono wanu, ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.


kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao.


Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzatuluka Ine kunka pakati pa Aejipito;


Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.


Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.


Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.


Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;


Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.


muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.


Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;


izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israele, potuluka iwo mu Ejipito;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa