Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 15:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Tsono Mose adapemphera dzolimba kwa Chauta, ndipo Chauta adamuwonetsa kamtengo. Mose adaponya kamtengoko m'madzi, ndipo madziwo adaleka kuŵaŵako. Kumeneko Chauta adapatsa anthuwo lamulo lokhazikika, ndipo adaŵayesanso komweko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino. Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:25
26 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka kunka ku magwero a madzi, nathiramo mchere, nati, Atero Yehova, Ndachiritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.


Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe chowawa.


Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva.


Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba.


Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.


Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.


Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai.


Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala.


Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa Iye kukhale pamaso panu, kuti musachimwe


Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo; koma Yehova ayesa mitima.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?


Nditabwera tsono, taonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri tsidya lino ndi lija.


Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa atulukira kudera la kum'mawa, natsikira kuchidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ake.


Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.


musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.


amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai.


Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israele, ndiwo onse amene sanadziwe nkhondo zonse za Kanani;


Amenewo anakhala choyesera Israele kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ake, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa