Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 22:23 - Buku Lopatulika

23 Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Iwe wokhala m'Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Inu amene mumakhala ku nyumba ya ku Lebanoni ija, amene mudamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza, mudzalira kwambiri pamene zoŵaŵa zidzakugwerani, zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni, amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza, mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani, zonga za mkazi pa nthawi yake yochira!

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:23
18 Mawu Ofanana  

Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?


Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.


Mau amveka pa mapiri oti see, kulira ndi kupempha kwa ana a Israele; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao.


Inu okhala mu Mowabu, siyani mizinda, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.


nuziti, Atero Ambuye Yehova, Chiombankhanga chachikulu ndi mapiko aakulu, ndi maphiphi aatali, odzala nthenga cha mathothomathotho, chinafika ku Lebanoni, nkutenga nsonga ya mkungudza,


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.


Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.


Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yake phindu loipa, kuti aike chisanja chake ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la choipa!


Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lake, nati, kwanu nkokhazikika, wamanga chisa chako m'thanthwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa