Ndipo kudzachitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaele; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu.
Amosi 1:3 - Buku Lopatulika Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo ankazunza anthu a ku Giliyadi mwankhanza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira za mano achitsulo, |
Ndipo kudzachitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaele; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu.
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israele, nawapereka m'dzanja la Hazaele mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele, masiku onsewo.
Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.
Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.
Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.
Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.
Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa choipa chanji chidzaoneka pansi pano.
Pakuti sapuntha mawere ndi chopunthira chakuthwa, ngakhale kuzunguniza njinga ya galeta pachitowe; koma amakulunga mawere ndi munsi, naomba chitowe ndi chibonga.
Taona, ndidzakuyesa iwe choombera tirigu chatsopano chakuthwa chokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.
Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa.
Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efuremu adzathyokathyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;
Chifukwa kuti mwana asanakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu;
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Mowabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza;
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza akaniza chilamulo cha Yehova, osasunga malemba ake; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato;
Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele;
ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Tiro ndi Sidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri.