Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 16:9 - Buku Lopatulika

9 Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono mfumu ya ku Asiriya idamvera Ahazi ndipo idakathira nkhondo Damasiko nilanda mzindawo ndi kupha Rezini. Anthu ake idaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Kiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mfumu ya ku Asiriya inamvera pokathira nkhondo mzinda wa Damasiko ndi kuwulanda. Anthu a mu mzindamo anawatumiza ku Kiri ndipo anapha Rezini.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 16:9
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi mizinda ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi mizinda yonse ya chuma ya Nafutali.


Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asiriya, osathandizidwa nazo.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wake anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukulu wa anthu ake, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israele, amene anamkantha makanthidwe aakulu.


Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemisi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi? Kodi Samariya sali ngati Damasiko?


Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mzinda, ndimo udzangokhala muunda wopasulidwa.


Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magaleta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa.


Zoonadi, Yehova, mafumu a Asiriya anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.


Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa.


Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza.


Chifukwa chake Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ake;


Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa