2 Mafumu 8:12 - Buku Lopatulika12 Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Tsono Hazaele adamufunsa kuti, “Mbuyanga, mukuliranji?” Iyeyo adayankha kuti, “Chifukwa ndikudziŵa zoipa zimene mudzaŵachita Aisraele. Mudzatentha malinga ao ankhondo ndipo mudzapha ankhondo ao ambiri. Mudzapondereza tiana tao, ndipo mudzang'amba akazi ao apakati.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Hazaeli anafunsa kuti, “Mbuye wanga mukulira chifukwa chiyani?” Elisa anayankha kuti, “Chifukwa ndikudziwa choyipa chimene udzachitira Aisraeli. Udzatentha mizinda yawo ya chitetezo, udzapha anyamata awo ndi lupanga, udzaphwanyitsa pansi makanda awo ndiponso udzatumbula mimba za akazi awo oyembekezera.” Onani mutuwo |
Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.