Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:7 - Buku Lopatulika

7 Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nthaŵi imeneyo Yehowahazi analibe gulu lankhondo lalikulu. Anali ndi asilikali a pa akavalo makumi asanu okha, magaleta khumi ndiponso asilikali oyenda pansi zikwi khumi, popeza kuti mfumu ya ku Siriya inali itaononga asilikali ambiri nkuŵaponderezeratu ngati fumbi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehowahazi sanatsale ndi ankhondo ambiri koma 50 okha okwera pa akavalo, magaleta khumi ndi asilikali oyenda pansi 10,000.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:7
17 Mawu Ofanana  

Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko, ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.


Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israele onse zikwi zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.


Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israele; ndipo Hazaele anawakantha m'malire onse a Israele,


Machitidwe ena tsono a Yehowahazi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.


Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo; ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.


Chifukwa chake upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asiriya, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.


Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.


Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m'chigwa chotsirizira mlandu.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo;


Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa