Mlaliki 11 - Buku LopatulikaTizichita zokoma lero lino posadziwa za mawa 1 Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri. 2 Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa choipa chanji chidzaoneka pansi pano. 3 Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwera pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo. 4 Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola. 5 Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse. 6 Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino. 7 Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa. 8 Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzachuluka. Zonse zilinkudza zili zachabe. Anyamata asangalale, koma adzikonzeretu pokumbukira imfa ikudza 9 Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi. 10 Chifukwa chake chotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi