Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 11:5 - Buku Lopatulika

5 Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 M'mene mzimu umaloŵera m'thupi la mwana m'mimba mwa mkazi wodwala, inu simudziŵa. Chonchonso ntchito ya Mulungu amene amapanga zonse, inu simungaidziŵe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo, kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi, momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 11:5
19 Mawu Ofanana  

Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.


Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.


amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.


Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.


Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova, zolingalira zanu nzozama ndithu.


Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.


Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.


Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.


Ndaona vuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo.


Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.


Chakutali ndi chakuyadi, adzachipeza ndani?


pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.


Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.


Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu.


Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa