Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
Afilipi 3:5 - Buku Lopatulika wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu ine ndidaumbalidwa pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditabadwa. Ndine wa mtundu wa Israele, wa fuko la Benjamini, Mhebri weniweni wobadwa mwa makolo achihebri. Kunena za Malamulo achiyuda, ndinali wa gulu la Afarisi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinachita mdulidwe pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditangobadwa. Ndine wa mtundu wa Israeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, kunena za malamulo, ndinali Mfarisi. |
Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.
A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.
chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.
Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira.
Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.
Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya.
Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.
Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;
Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.
Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.
Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.
Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.