Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Afilipi 3:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndinachita mdulidwe pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditangobadwa. Ndine wa mtundu wa Israeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, kunena za malamulo, ndinali Mfarisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pajatu ine ndidaumbalidwa pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditabadwa. Ndine wa mtundu wa Israele, wa fuko la Benjamini, Mhebri weniweni wobadwa mwa makolo achihebri. Kunena za Malamulo achiyuda, ndinali wa gulu la Afarisi.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 3:5
16 Mawu Ofanana  

Koma munthu wina amene anathawa, anabwera kudzamufotokozera Abramu Mhebri. Tsono Abramu ankakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya Mamre wa fuko la Aamori, mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri. Onsewa anali pa mgwirizano ndi Abramu.


Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako.


Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.”


Tsono momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, wantchito wa mkulu wa alonda. Ife tinamufotokozera maloto athu, ndipo anatitanthauzira malotowo. Munthu aliyense anamupatsa tanthauzo la loto lake.


Iye anayankha kuti, “Ndine Mhebri, ndipo ndimapembedza Yehova, Mulungu Wakumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.”


Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya,


Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe.


Ayi, vinyo watsopano ayenera kuthiridwa mʼmatumba a vinyo azikopa zatsopano.


“Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero.


Paulo atazindikira kuti ena mwa iwo anali Asaduki ndiponso ena anali Afarisi, anafuwula mʼbwalo muja kuti, “Abale anga, ine ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.”


Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku.


Ine ndikufunsa kuti kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Inenso ndine Mwisraeli, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini.


Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu.


Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?” Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa