Machitidwe a Atumwi 22:3 - Buku Lopatulika3 Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 “Inetu ndiye Myuda mbadwa ya ku Tariso, mzinda wa ku Silisiya, koma ndidaleredwa mu mzinda wa Yerusalemu mom'muno. Gamaliele ndiye anali mphunzitsi wanga amene adandiphunzitsa kwenikweni kusunga Malamulo a makolo athu. Ndipo ndinkalimbikira kwambiri pa za Mulungu, monga momwe mukuchitira nonsenu lero lino. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 “Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero. Onani mutuwo |