Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 40:15 - Buku Lopatulika

15 chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Inetu adachita chondiba, ndipo adabwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri. Tsono ngakhale kunoko, sindidachite kanthu kalikonse koti anditsekere nako m'ndende.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 40:15
19 Mawu Ofanana  

Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.


Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.


Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamutu panga;


Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira.


Anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anamgoneka mu unyolo;


pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.


Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m'dzanja lake, aphedwe ndithu.


Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.


Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?


Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.


Akampeza munthu waba mbale wake wina wa ana a Israele, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzichotsa choipacho pakati panu.


achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;


Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa