Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 40:14 - Buku Lopatulika

14 Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Komatu udzandikumbuke, zinthu zikadzakuyendera bwino. Chonde udzandikomere mtima ndi kutchula dzina langa kwa Farao, kuti ndidzatulule m'ndende muno.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma zako zikakuyendera bwino, udzandikumbukire ndi kundikomera mtima. Chonde ukandipepesere kwa Farao kuti anditulutse muno.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 40:14
9 Mawu Ofanana  

akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake.


Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero.


Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Saulo, kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?


Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.


Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m'mene mulowa Ufumu wanu.


Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko.


Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona,


mudzakhala opanda chakudodoma nacho, kapena chakusauka nacho mtima wa mbuye wanga, chakuti munakhetsa mwazi wopanda chifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera chilango ndipo Yehova akadzachitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukire mdzakazi wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa