Genesis 40:13 - Buku Lopatulika13 akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Pakangopita masiku atatu, Farao akutulutsa muno, akukhululukira, ndipo akubwezera pa ntchito yako. Tsono uzidzaperekera chikho kwa Farao monga momwe unkachitira kale. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Pakangopita masiku atatu, Farao adzakutulutsa muno. Udzaperekera zakumwa kwa Farao monga momwe umachitira poyamba. Onani mutuwo |
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;