Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 2:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe.

Onani mutuwo Koperani




Luka 2:21
9 Mawu Ofanana  

A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adule khungu la mwanayo.


Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.


ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.


Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.


Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.


Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya.


ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa