Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 5:38 - Buku Lopatulika

38 Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m'matumba atsopano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m'matumba atsopano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Ayi, vinyo watsopano ayenera kuthiridwa mʼmatumba a vinyo azikopa zatsopano.

Onani mutuwo Koperani




Luka 5:38
16 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.


Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.


Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m'matumba akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.


Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma.


Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.


ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa