Machitidwe a Atumwi 6:1 - Buku Lopatulika1 Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Masiku amenewo ophunzira aja ankachulukirachulukira. Koma Ayuda olankhula Chigriki anali ndi dandaulo pa Ayuda olankhula Chiyuda kuti akazi ao amasiye sankasamalidwa bwino pamene zachifundo za tsiku ndi tsiku zinkagaŵidwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku. Onani mutuwo |