Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 6:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono atumwi khumi ndi aŵiri aja adasonkhanitsa gulu lonse la ophunzira, naŵauza kuti, “Sibwino kuti ife tizisiya kulalika mau a Mulungu nkumayang'anira za chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 6:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?


Nchiyani tsono? Adzamva ndithu kuti wafika.


Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosatchulanso zifukwa zoti amneneze.


Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;


Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.


Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.


Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa