Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.
2 Samueli 8:18 - Buku Lopatulika Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Benaya, mwana wa Yehoyada, anali nduna yoyang'anira Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali ansembe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti; ndipo ana a Davide anali ansembe. |
Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.
Ndipo Yowabu anali woyang'anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;
Ndipo anatuluka namtsata anthu a Yowabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onse amphamvu; natuluka mu Yerusalemu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.
Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.
ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu.
Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.
Ndipo mfumu Solomoni anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye.
ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe,
ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,
Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.
Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabizeeli, wochita zachikulu, anapha ana awiri a Ariyele wa ku Mowabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya chipale chofewa.
ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu.
chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatambasulira Afilisti dzanja langa, ndi kulikha Akereti, ndi kuononga otsalira mphepete mwa nyanja.
Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko.
Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto.