Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 4:5 - Buku Lopatulika

5 ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Azariya mwana wa Natani ankayang'anira nduna zam'zigawo. Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi mlangizi wapadera wa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Azariya mwana wa Natani, anali woyangʼanira nduna za mʼzigawo; Zabudi mwana wa Natani, anali wansembe ndi bwenzi la mfumu;

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 4:5
17 Mawu Ofanana  

natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.


Chomwecho Husai bwenzi la Davide anadza m'mzindamo; ndipo Abisalomu anafika ku Yerusalemu.


Ndipo kunali pakudza kwa Abisalomu Husai Mwariki, bwenzi la Davide, Husai ananena ndi Abisalomu, Mfumu ikhale ndi moyo. Mfumu ikhale ndi moyo.


ndiponso Ira Myairi anali ansembe a Davide.


Maina a iwo anambadwira mu Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomoni,


mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga.


Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake.


ndi Ahisara anayang'anira banja la mfumu, ndi Adoniramu mwana wa Abida anali wamsonkho.


Ndipo Solomoni anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisraele onse, akufikitsira mfumu ndi banja lake zakudya; aliyense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa chaka.


ndi Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndi Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu;


Wokonda kuyera mtima, mfumu idzakhala bwenzi lake chifukwa cha chisomo cha milomo yake.


Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu.


ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa