2 Samueli 22:6 - Buku Lopatulika Zingwe za kumanda zinandizingira; misampha ya imfa inandifikira ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zingwe za kumanda zinandizingira; misampha ya imfa inandifikira ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthambo zakumanda zidandizeŵeza, misampha ya imfa idandikola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane. |
Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.
Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira.
yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.