Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 21:20 - Buku Lopatulika

20 Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 “Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, dziŵani kuti chiwonongeko chake chafika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 “Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi.

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:20
7 Mawu Ofanana  

Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.


Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)


Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:


Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;


Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike?


Ndi chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.


Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa