2 Samueli 22:10 - Buku Lopatulika Anaweramitsa miyambanso, natsika; ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anaweramitsa miyambanso, natsika; ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adang'amba thambo natsika pansi, mdima wabii unali ku mapazi ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda. |
Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.
Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu.
Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.
Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulire konse, ngati iwo amene sanatchedwe dzina lanu.
Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.
Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.
Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde paphiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.