Nahumu 1:3 - Buku Lopatulika3 Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; ndipo sadzalola kuti munthu wolakwa asalangidwe. Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake. Onani mutuwo |