Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
2 Samueli 2:18 - Buku Lopatulika Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yowabu, Abisai ndi Asahele, ana atatu aja a Zeruya, anali komweko. Asahele anali waliŵiro ngati insa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana atatu aamuna a Zeruya, Yowabu, Abisai ndi Asaheli anali komweko. Koma Asaheli anali waliwiro ngati insa. |
Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.
Ndipo Asahele anapirikitsa Abinere. Ndipo m'kuthamanga kwake sanapatukire kulamanja, kapena kulamanzere, pakutsata Abinere.
Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;
Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.
Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
Ndi Agadi ena anapatukira kwa Davide ku linga la m'chipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira chikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma mumapiri:
Wachinai wa mwezi wachinai ndiye Asahele mbale wa Yowabu, ndi pambuyo pake Zebadiya mwana wake; ndi m'chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.
Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mipata.
Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga, dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mphoka.
Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;
Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga, asanduliza mapazi anga ngati a mbawala, nadzandipondetsa pa misanje yanga.
Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.