Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 1:23 - Buku Lopatulika

23 Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo m'imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 “Saulo ndi Yonatani pa moyo wao anali okondedwa ndi okondwetsa, ndipo sadalekane ali moyo ngakhale pa imfa. Anali ndi liŵiro loposa la ziwombankhanga. Anali amphamvu kuposa mikango.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 “Sauli ndi Yonatani, pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima, ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe. Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga, anali ndi mphamvu zoposa mkango.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:23
14 Mawu Ofanana  

Ana aakazi inu a Israele, mulirire Saulo, amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa, amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu.


Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.


Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;


Ndi Agadi ena anapatukira kwa Davide ku linga la m'chipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira chikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma mumapiri:


Apitirira ngati zombo zaliwiro; ngati mphungu igudukira chakudya chake.


Mkango umene uposa zilombo kulimba, supatukira chinthu chilichonse;


M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana aakazi inu a ku Yerusalemu.


Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magaleta ake ngati kamvulumvulu; akavalo ake athamanga kopambana mphungu. Tsoka ife! Pakuti tapasuka.


Otilondola anaposa ziombankhanga za m'mlengalenga m'liwiro lao, anatithamangitsa pamapiri natilalira m'chipululu.


Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;


Ndipo amuna a pamzinda anati kwa Samisoni tsiku lachisanu ndi chiwiri, lisanalowe dzuwa, Chozuna choposa uchi nchiyani; ndi champhamvu choposa mkango nchiyani? Pamenepo ananena nao, Mukadapanda kulima ndi ng'ombe yanga, simukadatha kumasulira mwambi wanga.


Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.


Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa