Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 2:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Waliŵiro sadzatha kuthaŵa, wanyonga sadzakhalanso ndi mphamvu. Wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Munthu waliwiro sadzatha kuthawa, munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga, wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 2:14
9 Mawu Ofanana  

Koma maso a oipa adzagoma, ndi pothawirapo padzawasowa, ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.


Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa, mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona.


Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.


Ndipo abusa adzasowa pothawira, mkulu wa zoweta adzasowa populumukira.


Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m'mzinda usiku, panjira pamunda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira panjira ya kuchidikha.


Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;


wakufikitsa chionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, kuti chionongekocho chigwere linga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa