1 Mafumu 2:5 - Buku Lopatulika5 Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 “Kuwonjezera pamenepo, ukudziŵanso zoipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya adandichita, pakupha atsogoleri aŵiri a ankhondo a Aisraele aja, Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere. Kuteroko kunali kulipsira pa nthaŵi yamtendere magazi amene anthuwo adaakhetsa pa nthaŵi yankhondo. Koma tsopano ine pokhala mfumu, ndikusenza kuchimwa kwake ndi kuvala mlandu chifukwa cha magazi osachimwawo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 “Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake. Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.