2 Samueli 1:2 - Buku Lopatulika pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pa tsiku lachitatu lake, adangoona munthu akuchokera ku zithando zankhondo za Saulo, atavala zovala zong'ambika ndiponso atadzithira dothi kumutu. Munthuyo atafika kwa Davide, adadzigwetsa pansi, namlambira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo. |
Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake.
Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, na vala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri.
Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.
Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele.
Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka.
Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.
Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai Mwariki anadzakomana naye ali ndi malaya ake ong'ambika, ndi dothi pamutu pake.
Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.
muja munthu wina anandiuza kuti, Onani Saulo wamwalira, ndi kulingalira kuti alikubwera nao uthenga wabwino, ndinamgwira ndi kumupha ku Zikilagi, ndiyo mphotho yake ndinampatsa chifukwa cha uthenga wake.
Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka mu Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.
Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.
Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.
nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira fumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,
Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.
ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.
pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.
Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.
Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.
Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.
Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pabulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira,
Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake.
Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndachokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, Nkhondoyo idatani, mwana wanga?